Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 21:17-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Koma Abisai mwana wa Zeruya anamthandiza namkantha Mfliistiyo, namupha. Pomwepo anthu a Davide anamlumbirira iye nati, Inu simudzaturuka nafenso kunkhondo, kuti mungazime nyali ya Israyeli.

18. Ndipo kunali citapita ici, kunalinso nkhondo ndi Afilisti ku Gobu; pamenepo Sibekai Mhusati anapha Safi, ndiye wa ana a Rafa.

19. Ndipo panalinso nkhondo ndi Afilisti ku Gobu; ndipo Elhanani mwana wa Jare-oregimu wa ku Betelehemu anapha Goliate Mgiti, amene mtengo wa mkondo wace unanga mtanda wa woombera nsaru.

20. Ndipo panalinso nkhondo ku Gati, kumene kunali munthu wa msinkhu waukuru, amene anali nazo zala zisanu ndi cimodzi pa dzanja lonse, ndi pa phazi lonse zala zisanu ndi cimodzi kuwerenga kwa zonse ndiko makumi awiri ndi zinai; ndipo iyenso anambala ndi Rafa.

21. Ndipo pakutonza Israyeli iyeyu, Jonatani mwana wa Simeyi mbale wa Davide anamupha.

22. Awa anai anawabala ndi Rafa, ku Gati; ndipo anagwa ndi dzanja la Davide ndi la anyamata ace.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 21