Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 18:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Davide anawerenga anthu amene anali naye, nawaikira atsogoleri a zikwi ndi atsogoleri a mazana.

2. Davide natumiza anthu atawagawa magulu atatu, gulu limodzi aliyang'anire Yoabu, lina aliyang'anire Abisai, mwana wa Zeruya, mbale wa Yoabu, ndi lina aliyang'anire Itai Mgiti. Ndipo mfumu inanena ndi anthu, Zoonadi ine ndemwe ndidzaturuka limodzi ndi inu.

3. Koma anthuwo anati, Simudzaturuka ndinu; pakuti tikathawa sadzatisamalira ife; ngakhale limodzi la magawo awiri a ife likafa sadzatisamalira; koma inu mulingana ndi zikwi khumi a ife; cifukwa cace tsono nkwabwino kuti mutithandize kuturuka m'mudzi.

4. Ndipo mfumu inanena nao, Ndidzacita cimene cikomera inu. Mfumu niima pambali pa cipata, ndipo anthu onse anaturuka ali mazana, ndi zikwi.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 18