Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 14:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yoabu mwana wa Zeruya anazindikira kuti mtima wa mfumu unalunjika kwa Abisalomu.

2. Ndipo Yoabu anatumiza ku Tekowa, natenga kumeneko mkazi wanzeru, nanena naye, Ukokomezeke monga mfedwa, nubvale zobvala za pamaliro, osadzola mafuta, koma ukhale ngati munthu wamkazi wakulira akufa nthawi yaikuru.

3. Nulowe kwa mfumu, nulankhule nayo monga momwemo. Comweco Yoabu anampangira mau.

4. Ndipo pamene mkazi wa ku Tekowayo anati alankhule ndi mfumuyo, anagwa nkhope yace pansi namlambira, nati, Ndithandizeni mfumu.

5. Ndipo mfumuyo inanena naye, Usowanji? iye nayankha, Zoonadi ine ndine mkazi wamasiye, mwamuna wanga ana mwalira.

6. Ndipo mdzakazi wanu ndinali nao ana amuna awiri, ndipo awiriwa analimbana kumunda, panaboo wina wakuwaletsa, koma wina anakantha mnzace namupha.

7. Ndipo onani, cibale conse cinaukira mdzakazi wanu, ndi kuti, Upereke iye amene anakantha mbale wace, kuti timuphe cifukwa ca moyo wa mbale wace amene anamupha; koma pakutero adzaononga wolowa yemwe; comweco adzazima khara langa lotsala, ndipo sadzasiyira mwamuna wanga dzina kapena mbeu kunja kuno.

8. Ndipo mfumu inanena ndi mkaziyo, Pita ku nyumba yako, ndipo ndidzalamulira za iwe.

9. Ndipo mkazi wa ku Tekowayo ananena ndi mfumu, Mbuye wanga mfumu, mphulupulu ikhale pa ine ndi pa nyumba ya atate wanga; ndipo mfumu ndi mpando wacifumu wao zikhale zopanda cifukwa.

10. Ndipo mfumu inati, Ubwere naye kwa ine ali yense wakunena kanthu ndi iwe, ndipo iyeyo sadzakukhudzanso.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 14