Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 12:5-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Pamenepo mkwiyo wa Davide unayaka ndithu pa munthuyo, nati kwa Natani, Pali Yehova, munthu amene anacita ici, ayenera kumupha;

6. ndipo adzabwezera mwa mwana wa nkhosayo ena anai, cifukwa anacita ici osakhala naco cifundo.

7. Ndipo Natani ananena kwa Davide, Munthuyo ndi inu nomwe. Atero Yehova, Mulungu wa Israyeli, Ndinakudzoza ukhale mfumu ya Israyeli, ndinakupulumutsa m'dzanja la Sauli;

8. ndinakupatsa nyumba ya mbuye wako, ndi akazi a mbuye wako pa cifukato cako, ndinakupatsanso nyumba ya Israyeli ndi ya Yuda; ndipo zimenezi zikadakucepera ndikadakuonjezera zina zakuti zakuti.

9. Cifukwa ninji unapeputsa mau a Yehova ndi kucita cimene ciri coipa pamaso pace? Unakantha Uriya Mhiti ndi lupanga ndi kutenga mkazi wace akhale mkazi wako; ndipo unamupha iye ndi lupanga la ana a Amoni.

10. Cifukwa cace tsono lupanga silidzacoka pa nyumba yako nthawi zonse, popeza unandipeputsa Ine, nudzitengera mkazi wa Uriya Mhiti akhale mkazi wako.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 12