Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 10:10-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Koma anthu otsalawo anawapereka kwa Abisai mbale wace, amene anawandandalitsa ca kwa Amoni.

11. Ndipo iye anati, Aaramu akandipambana ine, udzandithandiza ndiwe, koma ana a Amoni akapambana iwe, tsono ndidzabwera ine kukuthandiza.

12. Ulimbike mtima, ndipo ticite camuna lero cifukwa ca anthu athu ndi midzi ya Mulungu wathu; Yehova nacite comkomera.

13. Comweco Yoabu ndi anthu amene anali naye anayandikira kuponyana nkhondo ndi Aaramu. Ndipo iwowa anathawa pamaso pace.

14. Ndipo pamene ana a Amoni anaona kuti Aaramu anathawa, iwonso anathawa pamaso pa Abisai, nalowa m'mudzimo. Ndipo Yoabu anabwera kucokera kwa ana a Amoni, nafika ku Yerusalemu.

15. Ndipo pamene Aaramu anaona kuti Aisrayeli anawathyola, anasonkhana pamodzi.

16. Ndipo Hadarezeri anatumiza mthenga nakatenga Aaramu a ku tsidya la cimtsinje; iwo nafika ku Helamu, ndi Sobaki kazembe wa khamu la nkhondo la Hadarezeri anawatsogolera.

17. Ndipo wina anauza Davide; iye nasonkhanitsa Aisrayeli onse, naoloka Yordano nafika ku Helemu, Ndipo Aaramu anandandalitsa nkhondo yao pa Davide namenyana naye.

18. Ndipo Aaramu anathawa pamaso pa Israyeli; Davide naphapo Aaramu apamagareta mazana asanu ndi awiri, ndi apakavalo zikwi makumi anai, nakantha Sobaki kazembe wa khamu lao, nafa iye pomwepo.

19. Ndipo pamene mafumu onse, otumikira Hadarezeri, anaona kuti Aisrayeli anawapambana, iwo anapangana mtendere ndi Aisrayeli, nawatumikira, Comweco Aaramu anaopa kuwathandizanso ana a Amoni.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 10