Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 4:18-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Ndipo Solomo anazipanga zipangizo izi zonse zocurukadi, pakuti kulemera kwace kwa mkuwa sikunayeseka.

19. Solomo anapanganso zipangizo zonse zinali m'nyumba ya Mulungu, guwa la nsembe lagolidi lomwe, ndi magome oikapo mkate woonekera;

20. ndi zoikapo nyali ndi nyali zace za golidi woona, zakuunikira monga mwa cilangizo cace cakuno ca moneneramo;

21. ndi maluwa, ndi nyali, ndi mbano zagolidi, ndiwo golidi wangwiro;

22. ndi zozimira nyali, ndi mbale zowazira, ndi zipande, ndi mbale za zofukiza za golidi woona; ndi kunena za polowera m'nyumba, zitseko zace za m'katimo za malo opatulikitsa, ndi zitseko za nyumbayi, ndiyo Kacisi, zinali zagolidi.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 4