Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 4:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Anapanganso guwa la nsembe lamkuwa, m'litali mwace mikono makumi awiri, ndi kupingasa kwace mikono makumi awiri, ndi msinkhu wace mikono khumi.

2. Anayenganso thawale losungunula la mikono khumi kukamwa, lozunguniza, ndi msinkhu wace mikono isanu; ndi cingweca mikono makumi atatu cinalizunguniza.

3. Ndi pansi pace panali mafanziro a ng'ombe zakulizinga khumi ku mkono umodzi, zakuzinga thawalelo pozungulira pace. Ng'ombezo zinali m'mizere iwiri, zinayengeka poyengedwa thawalelo.

4. Linasanjikika pa ng'ombe khumi ndi ziwiri, zitatu zinapenya kumpoto, ndi zitatu zinapenya kumadzulo, ndi zitatu zinapenya kumwela, ndi zitatu zinapenya kum'mawa; ndi thawale linasanjikika pamwamba pao, ndi nkholo zao zinayang'anana.

5. Ndi kucindikira kwace kunanga cikhato, ndi mlomo wace unasadamuka ngati mlomo wa comwera, ngati luwa la kakombo; analowamo madzi a mitsuko yaikuru zikwi zitatu.

6. Anapanganso mbiya zamphwamphwa khumi, naika zisanu ku dzanja lamanja, ndi zisanu ku dzanja lamanzere, kutsukiramo; za nsembe yopsereza anazitsuka m'menemo; koma thawale ndi la ansembe kusambiramo.

7. Ndipo anapanga zoikapo nyali khumi zagolidi, monga mwa ciweruzo cace; naziika m'Kacisi, zisanu ku dzanja lamanja, ndi zisanu ku dzanja lamanzere.

8. Anapanganso magome khumi, nawaika m'Kacisi, asanu ku dzanja lamanja, ndi asanu ku dzanja lamanzere. Napanga mbale zowazira zana limodzi zagolidi.

9. Anamanganso bwalo la ansembe, ndi bwalo lalikuru, ndi zitseko za kubwalo, nakuta zitseko zace ndi mkuwa.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 4