25. Koma Hezekiya sanabwezera monga mwa cokoma anamcitira, pakuti mtima wace unakwezeka; cifukwa cace unamdzera mkwiyo iye, ndi Yuda, ndi Yerusalemu.
26. Koma Hezekiya anadzicepetsa m'kudzikuza kwa mtima wace, iye ndi okhala m'Yerusalemu, momwemo mkwiyo wa Yehova sunawadzera masiku a Hezekiya.
27. Ndipo cuma ndi ulemu zinacurukira Hezekiya, nadzimangira iye zosungiramo siliva, ndi golidi, ndi timiyala ta mtengo wace, ndi zonunkhira, ndi zikopa, ndi zipangizo zokoma ziri zonse;
28. ndi nyumba zosungiramo zipatso za tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi zipinda za nyama iri yonse, ndi makola a zoweta.
29. Nadzimangiranso midzi, nadzionera nkhosa ndi ng'ombe zocuruka; pakuti Mulungu adampatsa cuma cambirimbiri.
30. Hezekiya yemweyo anatseka kasupe wa kumtunda wa madzi a Gihoni, nawapambutsa atsikire ku madzulo kwa mudzi wa Davide. Ndipo Hezekiya analemerera nazo nchito zace zonse.
31. Koma pokhala naye akazembe a akalonga a ku Babulo, amene anatumiza kwa iye kufunsira za codabwiza cija cidacitika m'dzikomo, Mulungu anamsiya, kumuyesa, kuti adziwe zonse za mumtima mwace.
32. Macitidwe ena tsono a Hezekiya, ndi nchito zace zokoma, taonani, zilembedwa m'masomphenya a Yesaya mneneri mwana wa Amozi, ndi m'buku la mafumu a Yuda ndi Israyeli.
33. Ndipo Hezekiya anagona ndi makolo ace, namuika polowerera ku manda a ana a Davide; ndi Ayuda onse ndi okhala m'Yerusalemu anamcitira ulemu pa imfa yace. Ndipo Manase mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.