Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 32:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Zitatha zinthu izi zokhulupirika, anadza Sanakeribu mfumu ya Asuri, nalowera Yuda, namangira midzi yamalinga misasa, nati adzigonjetsere iyi.

2. Ndipo pakuona Hezekiya kuti wadza Sanakeribu, ndi kuti nkhope yace inalunjikitsa kuyambana nkhondo ndi Yerusalemu,

3. anapangana ndi akuru ace ndi amphamvu ace, kutseka madzi a m'akasupe okhala kunja kwa mudzi; namthandiza iwo.

4. Nasonkhana anthu ambiri, natseka akasupe onse, ndi mtsinje woyenda pakati pa dziko, ndi kuti, Angafike mafumu a Asuri ndi kupeza madzi ambiri.

5. Ndipo analimbika mtima, namangitsa linga lonse mopasuka, nalikweza mpaka pansanja, ndi linga lina kunja kwace, nalimbitsa Milo m'mudzi wa Davide, napanga zida ndi zikopa zocuruka.

6. Naika akazembe a nkhondo alamulire anthu, nawasonkhanitsira kuli iye ku bwalo la ku cipata ca mudzi, nanena nao motonthoza mtima wao ndi kuti,

7. Limbani, mulimbike mtima, musaopa kapena ku tenga nkhawa pankhope pa mfumu ya Asuri ndi aunyinji okhala naye; pakuti okhala nafe acuruka koposa okhala naye;

8. pamodzi ndi iye pali dzanja la thupi lanyama; koma pamodzi ndi ife pali Yehova Mulungu wathu, kutithandiza ndi kutigwirira nkhondo. Ndipo anthu anacirikizika ndi mau a Hezekiya mfumu ya Yuda.

9. Pambuyo pace Sanakeribu mfumu ya Asuri, akali ku Lakisi ndi mphamvu yace yonse pamodzi naye, anatuma anyamata kwa Hezekiya mfumu ya Yuda, ndi kwa Ayuda onse okhala ku Yerusalemu, ndi kuti,

10. Atero Sanakeribu mfumu ya Asuri, Mutama ciani kuti mukhala m'linga m'Yerusalemu?

11. Sakukopani Hezekiya, kuti akuperekeni mufe nayo njala ndi ludzu, ndi kuti, Yehova Mulungu wathu adzatilanditsa m'dzanja la mfumu ya Asuri?

12. Sanaicotsa misanje yace ndi maguwa ace a nsembe Hezekiya yemweyo, nauza Yuda ndi Yerusalemu, ndi kuti, Mugwadire ku guwa la nsembe limodzi ndi kufukiza zonunkhira pamenepo?

13. Simudziwa kodi comwe ine ndi makolo anga tacitira anthu onse a m'maikomo? Kodi milungu ya mitundu ya anthu inakhoza konse kulanditsa dziko lao m'dzanja langa?

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 32