Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 31:15-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ndi omvera iye ndiwo Edeni, ndi Minyamini, ndi Yesuwa; ndi Semaya, Amariya, ndi Sekaniya, m'midzi ya ansembe, kugawira abale ao m'zigawo zao mokhulupirika, akuru monga ang'ono;

16. pamodzi ndi iwo oyesedwa mwa cibadwidwe ca amuna, kuyambira a zaka zitatu ndi mphambu, kwa ali yense amene adalowa m'nyumba ya Yehova, monga mwa nchito yace pa tsiku lace, kukacita za utumiki wao m'udikiro wao monga mwa zigawo zao;

17. ndi iwo oyesedwa mwa cibadwidwe ca ansembe mwa nyumba za makolo ao, ndi Alevi, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu m'udikiro mwao, monga mwa zigawo zao;

18. ndi iwo oyesedwa mwa cibadwidwe ca ana ao ang'ono onse, akazi ao, ndi ana ao amuna ndi akazi, mwa msonkhano wonse; pakuti m'kukhulupirika kwao anadzipatula akhale opatulika;

19. panalinso amuna mwa ana a Aroni ansembe, okhala m'minda ya kubusa kwa midzi yao, m'mudzi uli wonse, ochulidwa maina ao, agawire amuna onse mwa ansembe, ndi onse mwa Alevi, oyesedwa mwa cibadwidwe magawo ao.

20. Momwemo anacita Hezekiya mwa Yuda lonse nacita cokoma, ndi coyenera, ndi cokhulupirika, pamaso pa Yehova Mulungu wace.

21. Ndipo m'nchito iri yonse anaiyamba m'utumiki wa nyumba ya Mulungu, ndi m'cilamulo, ndi m'mauzo, kufuna Mulungu wace, anacita ndi mtima wace wonse, nalemerera nayo.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 31