Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 30:24-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Pakuti Hezekiya mfumu ya Yuda anapatsa msonkhano ng'ombe cikwi cimodzi, ndi nkhosa zikwi zisanu ndi ziwiri; ndi akuru anapatsa msonkhano ng'ombe cikwi cimodzi, ndi nkhosa zikwi khumi; ndipo ansembeambiri adadzipatula,

25. Ndi msonkhano wonse wa Yuda, pamodzi ndi ansembe ndi Alevi, ndi msonkhano wonse wocokera kwa Israyeli, ndi alendo ocokera ku dziko la Israyeli, ndi okhala m'Yuda, anakondwera.

26. Momwemo munali cimwemwe cacikuru m'Yerusalemu; pakuti kuyambira masiku a Solomo mwana wa Davide mfumu ya Israyeli simunacitika cotero m'Yerusalemu.

27. Pamenepo ansembe Alevi anauka, nadalitsa anthu; ndi mau ao anamveka, ndi pemphero lao lidakwera pokhala pace popatulika Kumwamba.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 30