Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 3:7-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Anamamatizanso kacisi, mitanda, ziundo, ndi makoma ace, ndi zitseko zace, ndi golidi; nalemba akerubi pamakoma.

8. Ndipo anamanga malo opatulikitsa, m'litali mwace monga mwa kupingasa kwa nyumba mikono makumi awiri, ndi kupingasa kwace mikono makumi awiri; naikuta ndi golidi wabwino wakufikira matalente mazana asanu ndi limodzi.

9. Ndi kulemera kwace kwa misomali ndiko masekeli makumi asanu a golidi. Ndipo anazikuta ndi golidi zipinda zosanjikizana.

10. Ndipo m'malo opatulikitsa anapanga akerubi awiri, anacita osema, nawakuta ndi golidi.

11. Ndi mapiko a akerubi m'litali mwace ndimo mikono makumi awiri; phiko la kerubi mmodzi mikono isanu, lojima khoma la nyumba; ndi phiko linzace mikono isanu, lokhudzana nalo phiko la kerubi wina.

12. Ndi phiko la kerubi wina mikono isanu lojima khoma la nyumba, ndi phiko linzace mikono isanu lolumikizana ndi phiko la kerubi wina.

13. Mapiko a akerubi awa anafunyululika mikono makumi awiri; ndipo anaima ndi mapazi ao, ndi, nkhope zao zinaloza kukhomo.

14. Ndipo anaomba nsaru yocinga ya thonje lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, naomberamo akerubi.

15. Ndipo anapanga ku khomo la nyumba nsanamira ziwiri za mikono makumi atatu mphambu ziwiri; ndi mutu unakhala pamwamba pa iri yonse ndiwo mikono isanu.

16. Napanga maunyolo onga a m'moneneramo, nawamanga pa mitu ya nsanamirazi, napanga makangaza zana limodzi, nawamanga pamaunyolo.

17. Ndipo anaimiritsa nsanamirazo pakhomo pa Kacisi; imodzi ku dzanja lamanja, ndi inzace ku dzanja lamanzere; nalicha dzina la iyi ya ku dzanja lamanja Yakini, ndi dzina la iyi ya ku dzanja lamanzere Boazi.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 3