Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 28:15-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Nanyamuka amuna ochulidwa maina, natenga andende, nabveka ausiwa onse mwa iwo ndi zofunkhazo, nawapatsa zobvala, ndi nsapato, nawadyetsa ndi kuwamwetsa, nawadzoza, nasenza ofoka ao onse pa aburu, nafika nao ku Yeriko, mudzi wa migwalangwa, kwa abale ao; nabwerera iwo kunka ku Samariya.

16. Nthawi yomweyi mfumu Ahazi anatumiza kwa mafumu a Asuri amthandize.

17. Pakuti Aedomu anadzanso, nakantha Yuda, natenga andende.

18. Afilisti omwe adagwa m'midzi ya kucidikha, ndi ya kumwela kwa Yuda, nalanda Betisemesi, ndi Azaloni, ndi Gederoti, ndi Soko ndi miraga yace, ndi Timna ndi miraga yace; nakhala iwo komweko.

19. Pakuti Yehova anacepetsa Yuda cifukwa ca Ahazi mfumu ya Israyeli; popeza iye anacita comasuka pakati pa Yuda, nalakwira Yehova kwambiri.

20. Ndipo Tigilati Pilesere mfumu ya Asuri anadza kwa iye, namsautsa osamlimbikitsa.

21. Pakuti Ahazi analandako za m'nyumba ya Yehova ndi za m'nyumba ya mfumu, ndi ya akalonga, nazipereka kwa mfumu ya Asuri, osathandizidwa nazo.

22. Ndipo nthawi ya nsautso yace anaonjeza kulakwira Yehova, mfumu Ahazi yemweyo.

23. Popeza anaphera nsembe milungu ya Damasiko yomkantha, nati, Popeza milungu ya mafumu a Aramu iwathandiza, ndiiphere nsembe, indithandize inenso. Koma inamkhumudwitsa iye, ndi Aisrayeli onse.

24. Ndipo Ahazi anasonkhanitsa zipangizo za m'nyumba ya Mulungu, naduladula zipangizo za m'nyumba ya Mulungu, natseka pa makomo a nyumba ya Yehova, nadzimangira maguwa a nsembe m'ngondya ziri zonse za Yerusalemu.

25. Ndi m'midzi iri yonse ya Yuda anamanga misanje ya kufukizira milungu yina, nautsa mkwiyo wa Yehova Mulungu wa makolo ace.

26. Macitidwe ena tsono, ndi njira zace zonse, zoyamba ndi zotsiriza, taonanani, zilembedwa m'buku la mafumu a Yuda ndi Israyeli.

27. Ndi Ahazi anagona ndi makolo ace, namuika m'mudzi wa Yerusalemu; pakuti sanadza naye ku manda a mafumu a Israyeli; ndipo Hezekiya mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 28