Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5
  6. 6
  7. 7
  8. 8
  9. 9
  10. 10
  11. 11
  12. 12
  13. 13
  14. 14
  15. 15
  16. 16
  17. 17
  18. 18
  19. 19
  20. 20
  21. 21
  22. 22
  23. 23
  24. 24
  25. 25
  26. 26
  27. 27
  28. 28
  29. 29
  30. 30
  31. 31
  32. 32
  33. 33
  34. 34
  35. 35
  36. 36

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Yotamu mfumu ya Yuda

1. Yotamu anali wa zaka makumi awiri, mphambu zisanu polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka khumi ndi zisanu ndi cimodzi; ndi dzina la mace ndiye Yerusa mwana wa Zadoki.

2. Ndipo anacita zoongoka pamaso pa Yehova, monga umo adacitira atate wace Uziya; pokhapo sanalowa m'Kacisi wa Yehova. Koma anthu anacitabe zobvunda.

3. Anamanga cipata ca kumtunda ca nyumba ya Yehova, ndi pa linga la Ofeli anamanga kwakukuru.

4. Namanga midzi m'mapiri a Yuda, ndi m'nkhalango anamanga nyumba zansanja, ndi nsanja zomwe.

5. Anayambananso ndi mfumu ya ana a Amoni, namgonjetsa, Ndi ana a Amoni anamninkha caka comweci matalente a siliva zana limodzi, ndi miyeso ya tirigu zikwi khumi, ndi ya barele zikwi khumi. Ana a Amoni anabwera nazo zomwezo kwa iye caka caciwiri ndi cacitatu comwe.

6. Momwemo Yotamu anakula mphamvu, popeza anakonza njira zace pamaso pa Yehova Mulungu wace.

7. Macitidwe ena tsono a Yotamu, ndi nkhondo zace zonse, ndi njira zace, taonani, zalembedwa m'buku la mafumu a Israyeli ndi Yuda.

8. Anali wa zaka makumi awiri mphambu zisanu polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka khumi mphambu zisanu ndi cimodzi.

9. Ndipo Yotamu anagona ndi makolo ace, namuika m'mudzi wa Davide; ndi Ahazi mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.