Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 26:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo anthu onse Ayuda anatenga Uziya, ndiye wa zaka khumi mphambu zisanu ndi cimodzi, namlonga ufumu m'malo mwa atate wace Amaziya.

2. Iye anamanga Eloti, naubweza kwa Yuda, mfumu itagona ndi makolo ace.

3. Uziya anali wa zaka khumi mphambu zisanu ndi cimodzi polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi asanu mphambu ziwiri; ndi dzina la mace ndiye Yekoliya wa ku Yerusalemu.

4. Nacita iye zoongoka pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adazicita atate wace Amaziya.

5. Ndipo iye anali munthu wakufuna Mulungu masiku a Zekariya, ndiye wozindikira masomphenya a Mulungu; ndipo masiku akufunira Yehova iye, Mulungu anamlemereza;

6. popeza anaturuka, nayambana ndi Afilisti, nagamula linga la Gati, ndi linga la Yabine, ndi linga la Asidodi; namanga midzi m'dziko la Asidodi, ndi mwa Afilisti.

7. Ndipo Mulungu anamthandiza poyambana ndi Afilisti, ndi Aarabu okhala m'Guribaala, ndi Ameuni.

8. Ndipo Aamoni anampatsa Uziya mitulo; ndi dzina lace linabuka mpaka polowera ku Aigupto; pakuti analil mbika cilimbikire.

9. Uziya anamanganso nsanja m'Yerusalemu pa cipata ca kungondya, ndi pa cipata ca kucigwa, ndi popindika linga; nazilimbikitsa.

10. Namanga nsanja m'cipululu, nakumba zitsime zambiri; popeza anali nazo zoweta zambiri; kumadambo, ndi kuzidikha; nakhala nao olima minda, ndi osunga mpesa kumapiri ndi ku nthaka yopatsa bwino; pakuti ndiye mlimi.

11. Uziya anali nalonso khamu la anthu a nkhondo, oturuka kunkhondo magulu; nawawerenga monga mwa mawerengedwe ao ndi dzanja la mlembi Yeyeli, ndi kapitao Maseya, monga anawauza Hananiya kazembe wina wa mfumu.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 26