Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 24:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Yoasi anali wa zaka zisanu ndi ziwiri polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi anai; ndi dzina la mace ndiye Zibiya wa ku Beereseba.

2. Ndipo Yoasi anacita zoongoka pamaso pa Yehova masiku onse a Yehoyada wansembe.

3. Ndipo Yehoyada anamtengera akazi awiri, nabala ana amuna ndi akazi.

4. Ndipo pambuyo pace mumtima mwa Yoasi munali cofuna kukonzanso nyumba ya Yehova.

5. Nasonkhanitsa ansembe ndi Alevi, nanena nao, Muturuke kumka ku midzi ya Yuda, ndi kusonkhanitsa kwa Aisrayeli onse ndarama zakukonzetsa nyumba ya Mulungu wanu caka ndi caka; ndipo inu fulumirani nayo nchitoyi. Koma Alevi sanafulumira nayo.

6. Ndipo mfumu inaitana Yehoyada mkuru wao, niti naye, Unalekeranji kuuza Alevi abwere nao kucokera m'Yuda ndi Yerusalemu msonkho wa Mose mtumiki wa Yehova, ndi wa msonkhano wa Israyeli, ukhale wa cihema ca umboni?

7. Pakuti ana a Ataliya mkazi woipa uja anathyola citseko ca nyumba ya Mulungu, natenga zopatulidwa zonse za nyumba ya Yehova kuzipereka kwa Baala.

8. Nilamulira mfumu, ndipo anapanga bokosi, naliika kunja ku cipata ca nyumba ya Yehova.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 24