Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 23:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Koma caka cacisanu ndi ciwiri Yehoyada anadzilimbitsa natenga atsogoleri a mazana, Azariya mwana wa Yeroamu, ndi Ismayeli mwana wa Yohanana, ndi Azariya mwana wa Obedi, ndi Maaseya mwana wa Adaya, ndi Elisafati mwana wa Zikiri, apangane naye pamodzi.

2. Ndipo iwo anayendayenda mwa Yuda, nasonkhanitsa Alevi m'midzi yonse ya Yuda, ndi akuru a nyumba za makolo m'Israyeli; nadza iwo ku Yerusalemu.

3. Ndipo msonkhano wonse unapangana pangano ndi mfumu m'nyumba ya Mulungu. Ndipo ananena nao, Taonani, mwana wa mfumu adzakhala mfumu monga Yehova ananena za ana a Davide.

4. Cimene muzicita ndi ici: limodzi la magawo atatu mwa inu olowera dzuwa la Sabata, la ansembe ndi Alevi, akhale olindirira pakhomo;

5. ndi limodzi la magawo atatu likhale ku nyumba ya mfumu; ndi limodzi la magawo atatu ku cipata ca maziko; ndi anthu onse akhale m'mabwalo a nyumba ya Yehova.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 23