11. Koma Yehosafati mwana wamkazi wa mfumu anatenga Yoasi mwana wa Ahaziya, namuba pakati pa ana a mfumu ophedwa, namlonga iye ndi mlezi wace m'cipinda cogonamo. Momwemo Yehosafati mwana wamkazi wa mfumu Yehoramu, mkazi wa Yehoyada wansembe (popeza ndiye mlongo wace wa Ahaziya), anambisira Ataliya, angamuphe.
12. Ndipo iye anali nao wobisika m'nyumba ya Mulungu zaka zisanu ndi cimodzi; nakhala Ataliya mfumu yaikazi ya dziko.