Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 20:26-37 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Ndi tsiku lacinai anasonkhana m'cigwa ca Beraka; pakuti pamenepo analemekeza Yehova; cifukwa cace anacha dzina lace la malowo, Cigwa ca Beraka, mpaka lero lino.

27. Pamenepo anabwerera amuna onse a Yuda, ndi a ku Yerusalemu, nawatsogolera ndi Yehosafati, kubwerera kumka ku Yerusalemu ndi cimwemwe; pakuti Yehova anawakondweretsa pa adani ao.

28. Ndipo anafika ku Yerusalemu ndi zisakasa, ndi azeze, ndi malipenga, ku nyumba ya Yehova.

29. Ndipo kuopsa kwa Mulungu kunagwera maufumu onse a m'maiko, pamene anamva kuti Yehova adayambana ndi adani a Israyeli.

30. Nucita bata ufumu wa Yehosafati; pakuti Mulungu wace anampumulitsira pozungulirapo.

31. Momwemo Yehosafati anakhala mfumu ya Yuda; anali wa zaka makumi atatu mphambu zisanu polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi awiri; ndi dzina la mace ndiye Azuba mwana wa Sili.

32. Ndipo anayenda m'njira ya Asa atate wace osapambukamo, nacita zoongoka pamaso pa Yehova.

33. Komatu misanje siinacotsedwa; popeza pamenepo anthu sadakonzere mitima yao kwa Mulungu wa makolo ao.

34. Macitidwe ena tsono adazicita Yehosafati, zoyamba ndi zotsiriza, taonani, zilembedwa m'buku la mau a Yehu mwana wa Hanani, wochulidwa m'buku la mafumu a Israyeli.

35. Zitathaizi, Yehosafati mfumu ya Yuda anaphatikana ndi Ahaziya mfumu ya Israyeli, yemweyo anacita moipitsitsa;

36. naphatikana naye kupanga zombo zomuka ku Tarisi, nazipanga zombozo m'Ezioni Gebere.

37. Pamenepo Eliezeri mwana wa Dodavahu wa Maresa ananenera kumtsutsa Yehosafati, ndi kuti, Popeza waphatikana ndi Ahaziya Yehova wapasula nchito zako. Ndipo zombo zinasweka zosakhoza kumuka ku Tarisi.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 20