Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 20:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo zitatha izi, kunacitika kuti ana a Moabu, ndi ana a Amoni, ndi ena pamodzi ndi Aamoni, anadza kuyambana nkhondo ndi Yehosafati.

2. Pamenepo anadza anthu akuuza Yehosafati, kuti, Ukudzerani unyinji waukuru wa anthu ocokera tsidya la nyanja ku Aramu; ndipo taonani, ali ku Hazazoni Tamara, ndiwo Engedi.

3. Ndipo Yehosafati anacita mantha, nalunjikitsa nkhope yace kufuna Yehova, nalalikira kusala mwa Ayuda onse.

4. Namemezedwa Yuda afunsire kwa Yehova, inde anacokera ku midzi yonse ya Yuda kufuna Yehova.

5. Ndipo Yehosafati anaima mu msonkhano wa Ayuda, ndi a ku Yerusalemu, ku nyumba ya Yehova, pakati pa bwalo latsopano;

6. nati, Yehova Mulungu wa makolo athu, Inu sindinu Mulungu wa m'Mwamba kodi? sindinu woweruza maufumu onse a amitundu kodi? ndi m'dzanja mwanu muli mphamvu yolimba; palibe wina wakulaka Inu.

7. Sindinu Mulungu wathu, amene munainga nzika za m'dziko muno pa maso pa ana anu Israyeli, ndi kulininkha kwa mbeu ya Abrahamu bwenzi lanu kosatha?

8. nakhala m'mwemo iwowa, nakumangirani m'mwemo malo opatulika a dzina lanu, ndi kuti,

9. Cikatigwera coipa, lupanga, ciweruzo, kapena mliri, kapena njala, tidzakhala ciriri pakhomo pa nyumba iyi, ndi pamaso panu, (pakuti m'nyumba muno muli dzina lanu), ndi kupfuulira kwa Inu m'kusauka kwathu; ndipo mudzamvera ndi kulanditsa.

10. Ndipo tsopano, taonani ana a Amoni, ndi Moabu, ndi a ku phiri la Seiri, amene simunalola Israyeli awalowere, pakuturuka iwo m'dziko la Aigupto, koma anawapambukira osawaononga;

11. tapenyani, m'mene atibwezera; kudzatiinga m'colowa canu, cimene munatipatsa cikhale colowa cathu.

12. Mulungu wathu, simudzawaweruza? pakuti mwa ife mulibe mphamvu yakulimbana nao aunyinji ambiri awa akutidzera; ndipo sitidziwa ngati tidzatani, koma maso athu ali kwa Inu.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 20