Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 19:2-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Naturuka Yehu mwana wa Hanani mlauli kukomana naye, nati kwa mfumu Yehosafati, Muyenera kodi kuthandiza oipa, ndi kukonda amene adana ndi Yehova? Cifukwa ca ici ukugwerani mkwiyo wocokera kwa Yehova.

3. Koma zapezeka zokoma mwa inu, popeza mwazicotsa zifanizo m'dzikomo, mwaluniikitsanso mtima wanu kufuna Mulungu.

4. Ndipo Yehosafati anakhala ku Yerusalemu, naturukiranso mwa anthu kuyambira ku Beereseba kufikira ku mapiri a Efraimu; nawabweza atsatenso Yehova Mulungu wa makolo ao.

5. Naika oweruza m'dziko, m'midzi yonse yamalinga ya m'Yuda, m'mudzi m'mudzi;

6. nati kwa oweruza, Khalani maso umo mucitira; pakuti simuweruzira anthu koma Yehova; ndipo ali nanu Iyeyu pakuweruza mlandu.

7. Ndipo tsono, kuopa Yehova kukhale pa inu, musamalire ndi kucita; pakuti palibe cosalungama kwa Yehova Mulungu wathu, kapena kusamalira monga mwa nkhope ya munthu, kapena kulandira mphatso.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 19