Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 17:8-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. ndi pamodzi nao Alevi, ndiwo Semaya, ndi Netaniya, ndi Zebadiya, ndi Asaheli, ndi Semiramoti, ndi Yonatani, ndi Adoniya, ndi Tobiya, ndi Tobadoniya, Alevi; ndi pamodzi nao Elisama ndi Yoramu, ansembe.

9. Ndipo anaphunzitsa m'Yuda ali nalo buku la cilamulo la Yehova, nayendayenda m'midzi yonse ya Yuda, naphunzitsa mwa anthu.

10. Ndipo kuopsa kwa Yehova kunagwera maufumu a maiko ozungulira Yuda; momwemo sanayambana ndi Yehosafati.

11. Ndipo Afilisti ena anabweca nazo kwa Yehosafati mitulo, ndi ndalama za msonkho; Aarabu omwe anabwera nazo kwa iye zoweta, nkhosa zamphongo zikwi zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu ndi awiri ndi atonde zikwi zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu ndi awiri.

12. Ndipo Yehosafati anakula cikulire, namanga m'Yuda nyumba zansanja, ndi midzi ya cuma.

13. Nakhala nazo nchito zambiri m'midzi ya Yuda, ndi anthu a nkhondo, ngwazi zamphamvu m'Yerusalemu.

14. Kuwerenga kwao monga mwa nyumba za atate ao ndiko: a Yuda, akuru a zikwi; Adina wamkuru, ndi pamodzi ndi iye ngwazi zamphamvu zikwi mazana atatu;

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 17