Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 16:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Caka ca makumi atatu mphambu zisanu ndi cimodzi ca Asa, Basa mfumu ya Israyeli anakwera kulimbana ndi Yuda, namangitsa Rama, kuwaletsa anthu asaturuke kapena kulowa kwa Asa mfumu ya Yuda.

2. Pamenepo Asa anaturutsa siliva ndi golidi ku cuma ca nyumba ya Yehova, ndi ca nyumba ya mfumu; nazitumiza kwa Benihadadi mfumu ya Aramu, yokhala ku Damasiko, ndi kuti,

3. Pakhale pangano pakati pa ine ndi inu, monga pakati pa atate wange ndi atate wanu; taonani, ndakutumizirani siliva ndi golidi; mukani, pasulani pangano lanu ndi Basa mfumu ya Israyeli, kuti andicokere.

4. Ndipo Benihadadi anamvera mfumu Asa natumiza akazembe a magulu ace a nkhondo ayambane ndi midzi ya Israyeli, nakantha Iyoni, ndi Dani, ndi Abelimaimu, ndi midzi yonse ya cuma ya Nafitali,

5. Ndipo kunali, pakumva ici Basa, analeka kumangitsa Rama, naleketsa nchito yace.

6. Pamenepo Asa mfumu anatenga Ayuda onse, ndipo anatuta miyala ya ku Rama, ndi mitengo yace, imene Basa adamanga nayo, namangira Geba ndi Mizipa.

7. Nthawi yomweyi Hanani mlauli anadza kwa Asa mfumu ya Yuda, nanena naye, Popeza mwatama mfumu ya Aramu, osatama Yehova Mulungu wanu, cifukwa cace khamu la nkhondo la mfumu ya Aramu lapulumuka m'dzanja lanu.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 16