Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 15:8-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndipo pakumva Asa mau awa, ndi cinenero ca Odedi mneneriyo, analimbika mtima, nacotsa zonyansazo m'dziko lonse la Yuda ndi Benjamini, ndi m'midzi adailanda ku mapiri a Efraimu; nakonza guwa la nsembe la Yehova lokhala pakhomo pa likole la Yehova.

9. Namemezaonse a m'Yuda ndi m'Benjamini, ndi iwo akukhala nao ocokera ku Efraimu, ndi Manase, ndi Simeoni; pakuti anamdzera ocuruka ocokera ku Israyeli, pamene anaona kuti Yehova Mulungu wace anali naye.

10. Ndipo anasonkhana ku Yerusalemu mwezi wacitatu, Asa atakhala mfumu zaka khumi ndi zinai.

11. Naphera Yehova nsembe tsiku lija za zofunkha adabwera nazo, ng'ombe mazana asanu ndi awiri, ndi nkhosa zikwi zisanu ndi ziwiri.

12. Nalowa cipangano cakufuna Yehova Mulungu wa makolo ao ndi mtima wao wonse, ndi moyo wao wonse;

13. ndi kuti yense wosafuna Yehova Mulungu wa Israyeli aphedwe, ngakhale wamng'ono kapena wamkuru, wamwamuna kapena wamkazi.

14. Ndipo analumbira kwa Yehova ndi mau akuru, ndi kupfuula ndi mphalasa ndi malipenga.

15. Ndipo Yuda yense anakondwera nalo lumbirolo; pakuti adalumbira ndi mtima wao wonse, namfunafuna ndi cifuno cao conse; ndipo anampeza; ndi Yehova anawapumulitsa pozungulirapo.

16. Maaka yemwe, mai wace wa Asa, mfumu, anamcotsa uyu asakhalenso mai wa ufumu, popeza anapanga fano loopsa la Asera; ndipo Asa analikha fano lace, naliphwanyaphwanya, nalitenthera ku mtsinje wa Kedroni.

17. Cinkana misanje siinacotsedwa m'Israyeli, mtima wa Asa unali wangwiro masiku ace onse.

18. Ndipo analowa nazo zopatulika za atate wace, ndi zopatulika zace zace, ku nyumba ya Mulungu; ndizo siliva, ndi golidi, ndi zipangizo.

19. Ndipo panalibenso nkhondo mpaka Asa atakhala mfumu zaka makumi atatu mphambu zinai.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 15