Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 15:6-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo anapasulidwa, mtundu wa anthu kupasula unzace, ndi mudzi kupasula mudzi; pakuti Mulungu anawabvuta ndi masautso ali onse.

7. Koma limbikani inu, manja anu asalende; pakuti ku nchito yanu kuli mphotho.

8. Ndipo pakumva Asa mau awa, ndi cinenero ca Odedi mneneriyo, analimbika mtima, nacotsa zonyansazo m'dziko lonse la Yuda ndi Benjamini, ndi m'midzi adailanda ku mapiri a Efraimu; nakonza guwa la nsembe la Yehova lokhala pakhomo pa likole la Yehova.

9. Namemezaonse a m'Yuda ndi m'Benjamini, ndi iwo akukhala nao ocokera ku Efraimu, ndi Manase, ndi Simeoni; pakuti anamdzera ocuruka ocokera ku Israyeli, pamene anaona kuti Yehova Mulungu wace anali naye.

10. Ndipo anasonkhana ku Yerusalemu mwezi wacitatu, Asa atakhala mfumu zaka khumi ndi zinai.

11. Naphera Yehova nsembe tsiku lija za zofunkha adabwera nazo, ng'ombe mazana asanu ndi awiri, ndi nkhosa zikwi zisanu ndi ziwiri.

12. Nalowa cipangano cakufuna Yehova Mulungu wa makolo ao ndi mtima wao wonse, ndi moyo wao wonse;

13. ndi kuti yense wosafuna Yehova Mulungu wa Israyeli aphedwe, ngakhale wamng'ono kapena wamkuru, wamwamuna kapena wamkazi.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 15