Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 15:2-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. ndipo anaturuka kukomana naye Asa, nanena naye, Mundimvere, Asa, ndi onse Ayuda ndi Abenjamini, Yehova ali nanu; mukakhala ndi Iye, mukamfuna Iye, mudzampeza; koma mukamsiya, adzakusiyani.

3. Masiku ambiri tsono Israyeli anakhala wopanda Mulungu woonayo, ndi wopanda wansembe wakuphunzitsa, ndi wopanda cilamulo;

4. koma pamene anatembenukira kwa Yehova Mulungu wa Israyeli m'kusautsidwa kwao, ndi kumfuna, anampeza.

5. Ndipo nthawi zija panalibe mtendere kwa iye wakuturuka, kapena kwa iye wakulowa, koma mabvuto akuru anagwera onse okhala m'maikomo.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 15