Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 10:14-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. nalankhula nao monga umo anampangira acinyamata, ndi kuti, Atate wanga analemeretsa goli lanu, koma ine ndidzaonjezerapo; atate wanga anakukwapulani ndi zikoti, koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.

15. Momwemo mfumu siinamvera anthuwo; pakuti kusinthaku kudafuma kwa Mulungu, kuti Yehova akhazikitse mau ace, amene ananenetsa Ahiya wa ku Silo kwa Yerobiamu mwana wa Nebati.

16. Ndipo pakuona Aisrayeli onse kuti mfumu sinawamvera anthuwo, anamyankha mfumu, ndi kuti, Tiri naye ciani Davide? inde tiribe colowa m'mwana wa Jese; tiyeni kwathu, Aisrayeli inu; yang'anira nyumba yako tsopano, Davide. Momwemo Aisrayeli onse anamuka ku mahema ao.

17. Koma za ana a Israyeli okhala m'midzi ya Yuda, Rehabiamu anakhalabe mfumu yao.

18. Pamenepo Rehabiamu mfumu inatuma Hadoramu woyang'anira thangata; koma ana a Israyeli anamponya miyala, nafa. Ndipo Rehabiamu mfumu anafulumira kukwera pa gareta wace kuthawira ku Yerusalemu.

19. Motero Israyeli anapandukana nayo nyumba ya Yuda mpaka lero lino.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 10