Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 8:14-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ndipo anacoka kwa Elisa, nadza kwa mbuye wace; ameneyo ananena naye, Anakuuza ciani Elisa? Nati iye, Anandiuza kuti mudzacira ndithu.

15. Ndipo kunali m'mawa mwace, anatenga cimbwi, nacibviika m'madzi, naciphimba pankhope pa mfumu, nifa; ndipo Hazaeli analowa ufumu m'malo mwace.

16. Ndipo caka cacisanu ca Yoramu mwana wa Ahabu mfumu ya Israyeli, pokhala Yehosafati mfumu ya Yuda, Yehoramu mwana wa Yehosafati analowa ufumu.

17. Ndiye wa zaka makumi atatu ndi ciwiri polowa ufumu wace, nacita ufumu zaka zisanu ndi zitatu ku Yerusalemu.

18. Nayenda m'njira ya mafumu a Israyeli, m'mene inacitira nyumba ya Ahabu; pakuti mkazi wace ndiye mwana wa Ahabu, nacita iye coipa pamaso pa Yehova.

19. Koma Yehova sanafuna kuononga Yuda, cifukwa ca Davide mtumiki wace monga adamuuza, kuti adzampatsa nyali ya kwa ana ace kosalekeza.

20. Masiku ace Aedomu anapanduka ku ulamuliro wa Yuda, nadziikira mfumu okha.

21. Pamenepo Yoramu anaoloka kumka ku Zairi, ndi magareta ace onse pamodzi naye; nauka iye usiku, nakantha Aedomu akumzinga ndi nduna za magareta, nathawira anthu ku mahema ao.

22. Motero Aedomu anapanduka ku ulamuliro wa Yuda mpaka lero lino. Ndipo Alibina anapanduka nthawi yomweyi.

23. Ndi macitidwe ena a Yoramu, ndi zonse anazicita, sizinalembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda.

24. Nagona Yoramu ndi makolo ace, naikidwa pamodzi ndi makolo ace m'mudzi wa Davide; ndipo Ahaziya mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 8