Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 4:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo wina wa akazi a ana a aneneri anapfuula kwa Elisa, ndi kuti, Mnyamata wanu, mwamuna wanga wafa; mudziwa kuti mnyamata wanu anaopa Yehova; ndipo wafika wamangawa kunditengera ana anga awiri akhale akapolo ace.

2. Ndipo Elisa anati kwa iye, Ndikucitire ciani? undiuze m'nyumba mwako muli ciani? Nati, Mdzakazi wanu alibe kanthu m'nyumba, koma mtsuko wa mafuta.

3. Pamenepo anati, Kabwereke zotengera kwina kwa anansi ako onse, zotengera zopanda kanthu, zisakhale pang'ono.

4. Nulowe, uudzitsekere wekha ndi ana ako amuna ndi kutsanulira m'zotengera zonsezi, nuike padera zodzalazo.

5. Pamenepo anamcokera, nadzitsekera yekha ndi ana ace amuna; iwo namtengera zotengerazo, iye namatsanulira.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 4