Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 3:23-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. nati, Uja ndi mwazi, atha kuonongana mafumu aja, anakanthana wina ndi mnzace; ndipo tsopano, tiyeni Amoabu inu, tikafunkhe.

24. Ndipo pamene anafika ku misasa ya Israyeli, Aisrayeli ananyamuka, nakantha Amoabu, nathawa iwo pamaso pao; ndipo analowa m'dziko ndi kukantha Amoabu.

25. Napasula midzi, naponya yense mwala wace panthaka ponse pabwino, naidzaza, nafotsera zitsime zonse zamadzi, nagwetsa mitengo yonse yabwino, kufikira anasiya miyala yace m'Kirihasereti mokha; koma oponya miyala anauzinga, naukantha.

26. Ndipo ataona mfumu ya Moabu kuti nkhondo idamlaka, anapita nao anthu mazana asanu ndi awiri akusolola lupanga, kupyola kufikira kwa mfumu ya Edomu, koma sanakhoza.

27. Pamenepo anagwira mwana wace wamwamuna woyamba amene akadakhala mfumu m'malo mwace, nampereka nsembe yopsereza palinga. Ndipo anakwiyira Israyeli kwambiri; potero anamcokera, nabwerera ku dziko lao.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 3