Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 25:15-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ndi zoparira moto, ndi mbale zowazira za golidi yekha yekha, ndi zasiliva yekha yekha, mkuru wa asilikari anazicotsa.

16. Nsanamira ziwiri, thawale limodzi, ndi maphakawo adazipangira nyumba ya Yehova Solomo, mkuwa wa zipangizo izi zonse sanakhoza kuyesa kulemera kwace.

17. Msinkhu wace wa nsanamira imodzi ndiwo mikono khumi mphambu isanu ndi itatu, ndi pamwamba pace mutu wamkuwa; ndi msinkhu wace wa mutuwo ndiwo mikono itatu, ndi ukonde, ndi makangaza pamutu pouzinga, zonse zamkuwa; ndi nsanamira inzace inali nazo zomwezo pamodzi ndi ukonde.

18. Ndipo mkuru wa olindirira anatenga Seraya wansembe wamkulu, ndi Zefaniya wansembe waciwiri, ndi olindira pakhomo atatu;

19. natenga m'mudzimo mdindo woikidwa woyang'anira ankhondo; ndi anthu asanu a iwo openya nkhope ya mfumu opezeka m'mudzimo; ndi mlembi, kazembe wa nkhondo wolembera anthu a m'dziko; ndi anthu a m'dziko makumi asanu ndi limodzi opezeka m'mudzimo.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 25