Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 21:16-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Ndiponso Manase anakhetsa mwazi wambiri wosacimwa mpaka anadzaza m'Yerusalemu monsemo, osawerenga kulakwa kwace analakwitsa nako Yuda, ndi kucita coipa pamaso pa Yehova.

17. Macitidwe ena tsono a Manase, ndi zonse anazicita, sizilembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda?

18. Nagona Manase ndi makolo ace, naikidwa m'munda wa nyumba yace, m'munda wa Uza, nakhala mfumu m'malo mwace Amoni mwana wace.

19. Amoni anali wa zaka makumi awiri mphambu ziwiri polowa iye ufumu wace, nakhala mfumu zaka ziwiri m'Yerusalemu; ndi dzina la mace ndiye Mesulemeti mwana wa Haruzi wa ku Yotiba.

20. Nacita iye coipa pamaso pa Yehova, monga umo amacitira Manase atate wace.

21. Nayenda iye m'njira monse anayendamo atate wace, natumikira mafano anawatumikira atate wace, nawagwadira;

22. nasiya Yehova Mulungu wa makolo ace, sanayenda m'njira ya Yehova.

23. Ndipo anyamata ace a Amoni anamcitira ciwembu, napha mfumuyo m'nyumba yace yace.

24. Koma anthu a m'dzikomo anapha onse akumcitira ciwembu mfumu Amoni; ndipo anthu a m'dzikomo anamlonga ufumu Yosiya mwana wace m'malo mwace.

25. Macitidwe ena tsono a Amoni adawacita, salembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda?

26. Naikidwa iye m'manda mwace m'munda wa Uza; nakhalamfumum'malo mwace Yosiya mwana wace.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 21