1. Manase anali wa zaka khumi ndi ziwiri polowa iye ufumu wace, nakhala mfumu zaka makumi asanu ndi zisanu m'Yerusalemu; ndi dzina la mace ndiye Hefisiba.
2. Ndipo anacita coipa pamaso pa Yehova, monga mwa zonyansa za amitundu amene Yehova anawaingitsa pamaso pa ana a Israyeli.
3. Pakuti anamanganso misanje, imene Hezekiya atate wace adaiononga; nautsira Baala maguwa a nsembe, nasema cifanizo, monga anacita Ahabu mfumu ya Israyeli, nagwadira khamu lonse la kuthambo, nalitumikira.
4. Namanga iye maguwa a nsembe m'nyumba ya Yehova imene Yehova adainenera kuti, M'Yerusalemu ndidzaika dzina langa.
5. Nalimangira khamu lonse la kuthambo maguwa a nsembe m'mabwalo awiri a nyumba ya Yehova.
6. Napititsa mwana wace pamoto, naombeza maula, nacita zanyanga, naika obwebweta ndi openda; anacita zoipa zambiri pamaso pa Yehova kuutsa mkwiyo wace.