Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 2:14-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ndipo anatenga copfunda ca Eliya cidamtayikiraco, napanda madziwo, nati, Ali kuti Yehova Mulungu wa Eliya? Ndipo atapanda madziwo anagawikana kwina ndi kwina, naoloka Elisa.

15. Ndipo pamene anampenya ana a aneneri okhala ku Yeriko pandunji pace, anati, Mzimu wa Eliya watera pa Elisa. Ndipo anadza kukomana naye, nadziweramitsa pansi kumaso kwace.

16. Ndipo ananena naye, Taonani, tsono anyamata anufe tiri nao amuna makumi asanu amphamvu, amuke kukafuna mbuye wanu; kapena wamkweza mzimu wa Yehova ndi kumponya pa phiri lina, kapena m'cigwa dna. Koma anati, Musatumiza.

17. Koma anamuumiriza kufikira anacita manyazi; pamenepo anati, Tumizani. Motero anatumiza amuna makumi asanu, namfunafuna iwo masiku atatu, osampeza.

18. Nabwerera kwa iye ali cikhalire ku Yeriko, ndipo anati kwa iwo, Kodi sindinanena nanu, Musamuka?

19. Ndipo amuna a kumudzi anati kwa Elisa, Taonani, pamudzi pano mpabwino, monga umo aonera mbuye wanga; koma madzi ndi oipa, ndi nthaka siibalitsa.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 2