Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 18:6-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Pakuti anaumirira Yehova osapambuka pambuyo pace, koma anasunga malamulo amene Yehova adawalamulira Mose.

7. Ndipo Yehova anali naye, nacita iye mwanzeru kuli konse anamukako, napandukira mfumu ya Asuri osamtumikira.

8. Anakantha Afilisti mpaka Gaza ndi malire ace, kuyambira nsanja ya olonda mpaka mudzi walinga.

9. Ndipo kunali caka cacinai ca mfumu Hezekiya, ndico caka cacisanu ndi ciwiri ca Hoseya mwana wa Ela mfumu ya Israyeli Salimanezeri mfumu ya Asuri anakwerera Samariya, naumangira misasa.

10. Pakutha pace pa zaka zitatu anaulanda, ndico caka cacisanu ndi cimodzi ca Hezekiya, ndico caka cacisanu ndi cinai ca Hoseya mfumu ya Israyeli analanda Samariya.

11. Ndipo mfumu ya Asuri anacotsa Aisrayeli kumka nao ku Asuri, nawakhalitsa m'Hala, ndi m'Habori, ku mtsinje wa Gozani, ndi m'midzi ya Amedi;

12. cifukwa sanamvera mau a Yehova Mulungu wao, koma analakwira cipangano cace, ndico zonse anazilamulira Mose mtumiki wa Yehova; sanazimvera kapena kuzicita.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 18