Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 18:33-37 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

33. Kodi mlungu uli wonse wa amitundu walanditsa dziko lace m'dzanja la mfumu ya Asuri ndi kale lonse?

34. Iri kuti milungu ya Hamati, ndi ya Aripadi? iri kuti milungu ya Sefaravaimu, kapena Hena, ndi Iva? Kodi yalanditsa Samariya m'dzanja langa?

35. Ndi yiti mwa milungu yonse ya maiko inalanditsa maiko ao m'dzanja langa, kuti Yehova adzalanditsa Yerusalemu m'dzanja langa?

36. Koma anthuwo anakhala cete osamyankha mau; pakuti lamulo la mfumu ndilo kuti, Musamuyankha.

37. Pamenepo Eliyakimu mwana wa Hilikiya woyang'anira nyumba, ndi Sebina mlembi, ndi Yoa mwana wa Asafu wolembera mbiri, anadza kwa Hezekiya ndi zobvala zao zong'ambika, namuuza mau a kazembeyo.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 18