Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 17:30-41 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

30. Ndipo anthu a Babulo anapanga Sukoti Bemoti, ndi anthu a Kuta anapanga Nerigali, ndi anthu a Hamati anapanga Asima,

31. ndi Aava anapanga Nibazi ndi Tarataka; ndi a Sefaravaimu anawatentha ana ao m'moto kwa Adrameleki, ndi Anameleki, milungu ya Asefaravaimu.

32. Popeza anaopanso Yehova, anadziikira mwa iwo okha ansembe a misanje, ndiwo anaperekera nsembe m'nyumba za misanje.

33. Amaopa Yehova, namatumikiranso milungu yao, monga mwa miyambo ya amitundu anawacotsako.

34. Mpaka lero lino acita monga mwa miyambo yoyambayi; saopa Yehova, sacita monga mwa malemba ao, kapena maweruzo ao, kapena cilamulo, kapena coikika adacilamulira Yehova ana a Yakobo, amene anamucha Israyeli,

35. ndiwo amene Yehova adapangana nao, nawalamulira, ndi kuti, Musamaopa milungu yina, kapena kuigwadira, kapena kuitumikira, kapena kuiphera nsembe;

36. koma Yehova amene anakukwezani kukuturutsani m'dziko la Aigupto ndi mphamvu yaikuru, ndi dzanja lotambasuka, Iyeyu muzimuopa, ndi Iyeyu muzimgwadira, ndi Iyeyu muzimphera nsembe;

37. ndi malemba, ndimaweruzo, ndi cilamulo, ndi coikika anakulemberani muzisamalira kuzicita masiku onse, nimusamaopa milungu: yina;

38. ndi cipangano ndinacicita nanu musamaciiwala, kapena kuopa milungu yina iai;

39. koma Yehova Mulungu wanu muzimuopa, nadzakulanditsani Iyeyu m'dzanja la adani anu onse.

40. Koma sanamvera, nacita monga mwa mwambo wao woyamba.

41. Ndipo amitundu awa anaopa Yehova, natumikira mafano ao osema; ana ao omwe, ndi zidzukulu zao zomwe, monga anacita makolo ao, momwemo iwo omwe mpaka lero lino.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 17