Pamenepo mfumu ya Asuri analamulira, kuti, Mukani naye komweko wina wa ansembe munawacotsako, nakakhale komweko, akawalangize makhalidwe a Mulungu wa dzikoli.