Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 15:28-34 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. Nacita coipa pamaso pa Yehova: osaleka zolakwa za Yerobiamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israyeli,

29. Masiku a Peka mfumu ya Israyeli anadza Tigilati Pilesere mfumu ya Asuri, nalanda Ijoni, ndi Abeli-BeteMaaka, ndi Yanoa, ndi Kedesi, ndi Hazori, ndi Gileadi, ndi Galileya, dziko lonse la Nafitali; nawatenga andende kumka nao ku Asuri.

30. Ndipo Hoseya mwana wa Ela anamcitira ciwembu Peka mwana wa Remaliya, namkantha, namupha, nakhala mfumu m'malo mwace caka ca makumi awiri ca Yotamu mwana wa Uziya.

31. Macitidwe ena tsono a Peka, ndi zonse anazicita, taonani, zalembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli.

32. Caka caciwiri ca Peka mwana wa Remaliya mfumu ya Israyeli, Yotamu mwana wa Uziya mfumu ya Yuda analowa ufumu wace.

33. Ndiye wa zaka makumi awiri mphambu: zisanu polowa ufumu wace, nakhalamfumu zaka khumi ndi zisanu ndi cimodzi m'Yerusalemu; ndipo dzina la mace ndiye Yerusa mwana wa Zadoki.

34. Nacita iye zoongoka pamaso pa Yehova; anacita monga mwa zonse anazicita atate; wace Uziya.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 15