Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 15:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Caka ca makumi awiri mphambu zisanu ndi ziwiri ca Yerobiamu mfumu ya Israyeli, Azariya mwana wa Amaziya mfumu ya Yuda analowa ufumu wace.

2. Anali wa zaka khumi ndi zisanu ndi cimodzi polowa ufumu wace, nakhala mfumu zaka makumi asanu mphambu ziwiri m'Yerusalemu; ndi dzina la mace ndiye Yekoliya wa ku Yerusalemu.

3. Nacita iye zoongoka pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adazicita atate wace Amaziya.

4. Komatu sanaicotsa misanje; anthu anapherabe nsembe, nafukiza pamisanje.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 15