Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 14:11-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Koma Amaziya sanamvera. Motero anakwera Yoasi mfumu ya Israyeli, ndipo iye ndi Amaziya mfumu ya Yuda anapenyana maso ku Betisemesi, ndiwo wa Yuda.

12. Nakanthidwa Yuda pamaso pa Israyeli, nathawira yense kuhema kwace.

13. Ndipo Yoasi mfumu ya Israyeli anagwira Amaziya mfumu ya Yuda, mwana wa Yoasi mwana wa Ahaziya, ku Betisemesi, nadza ku Yerusalemu, nagamula linga la Yerusalemu kuyambira cipata ca Efraimu kufikira cipata ca kungondya, mikono mazana anai.

14. Natenga golidi ndi siliva yense, ndi zotengera zonse anazipeza m'nyumba ya Yehova, ndi ku cuma ca m'nyumba ya mfumu, acikole omwe; nabwera kumka ku Samariya,

15. Macitidwe ena tsono a Yoasi adazicita, ndi mphamvu yace, ndi umo analimbana naye Amaziya mfumu ya Yuda, sizilembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli?

16. Nagona Yoasi ndi makolo ace, namuika m'Samariya pamodzi ndi mafumu a Israyeli; nakhala mfumu m'malo mwace Yerobiamu mwana wace.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 14