Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 11:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamene Ataliya mace wa Ahaziya anaona kuti mwana wace wafa, ananyamuka, naononga mbeu yonse yacifumu.

2. Koma Yoseba mwana wa mfumu Yoramu, mlongo wace wa Ahaziya, anatenga Yoasi mwana wa Ahaziya, namuba pakati pa ana a mfumu akuti aphedwe, iye ndi mlezi, nawaika m'cipinda cogonamo; nambisira Ataliya, ndipo sanaphedwa.

3. Nakhala naye wobisika m'nyumba ya Yehova zaka zisanu ndi cimodzi; ndipo Ataliya anakhala mfumu ya dziko.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 11