Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 1:3-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Koma mthenga wa Yehova anati kwa Eliya wa ku Tisibe, Nyamuka, kwera kukomana ndi mithenga ya mfumu ya Samariya, nunene nayo, Kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israyeli, kuti mukafunsira kwa Baala Zebubu mulungu wa ku Ekroni?

4. Cifukwa cace atero Yehova, Sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu. Nacoka Eliya.

5. Ndipo mithenga inabwerera kwa iye, nanena nayo, Mwabwerera cifukwa ninji?

6. Ndipo inanena naye, Munthu anakwera kukomana nafe, nati kwa ife, Kabwerereni kwa mfumu imene inakutumani inu, nimunene nayo, Atero Yehova, Kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israyeli, kuti ulikutuma kukafunsira kwa Baala Zebubu mulungu wa ku Ekroni? Cifukwa cace sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu.

7. Ndipo iye ananena nayo, Nanga maonekedwe ace a munthu anakwerayo kukomana nanu, nanena nanu mau awa, ndi otani?

8. Ninena naye, Ndiye munthu wobvala zaubweya, namangira m'cuuno mwace ndi lamba lacikopa. Nati iye, Ndiye Eliya wa ku Tisibe.

9. Pamenepo mfumu inatuma kwa iye asilikari makumi asanu ndi mtsogoleri wao. Iye nakwera kumka kwa Eliya; ndipo taonani, analikukhala pamwamba pa phiri. Ndipo analankhula naye, Munthu wa Mulungu iwe, mfumu ikuti, Tsika.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 1