12. Pamenepo Samueli anatenga mwala nauimika pakati pa Mizipa ndi Seni, naucha dzina lace. Ebenezeri, nati, Kufikira pano Yehovaanatithandiza.
13. Comweco anagonjetsa Afilisti, ndino iwo sanatumphanso malire a Israyeli ndipo dzanja la Yehova linasautsa Afilisti masiku onse a Samueli.
14. Ndipo midzi ya Israyeli imene Afilisti adailanda kale inabwezedwa kwa Aisrayeli, kuyambira ku Ekroni kufikira ku Gati; ndi Aisrayeli analanditsa miraga yao m'manja a Afilisti. Ndipo pakati pa Aisrayeli ndi Aamori panali mtendere;
15. ndipo Samueli anaweruza Israyeli masiku onse a moyo wace.
16. Ndipo anayenda cozungulira caka ndi caka ku Beteli, ndi ku Giligala, ndi ku Mizipa; naweruza Israyeli m'malo onse amenewa.
17. Ndipo anabwera ku Rama, pakuti nyumba yace inali kumeneko; ndipo pamenepo anaweruza Israyeli; namangapo guwa la nsembe la Yehova.