Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 31:2-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Ndipo Afilisti anapitikitsa, osawaleka Sauli ndi ana ace; ndipo Afilisti anapha Jonatani, ndi Abinadabu, ndi Malikisua, ana a Sauli.

3. Ndipo nkhondoyo inamkulira Sauli kwambiri, oponya mibvi nampeza; ndipo iye anasautsika kwakukuru cifukwa ca oponya mibviyo.

4. Tsono Sauli ananena ndi wonyamula zida zace, Solola lupanga lako, undipyoze nalo; kuti osadulidwa awa angabwere ndi kundipyoza, ndi kundiseka, Koma woo nyamula zida zace anakana; cifukwa anaopa ndithu. Cifukwa cace Sauli anatenga lupanga lace naligwera.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 31