Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 30:23-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Davide nati, Simudzatero, abale anga inu, ndi zimene anatipatsa ife Yehova, amene anatisunga, napereka m'dzanja lathu khamu lija linadza kumenyana nafe.

24. Ndipo ndani adzabvomerezana nanu mrandu uwu? Pakuti monga gawo lace la iye wakumuka kunkhondoko, momwemo lidzakhala gawo lace la iye wakukhala ndi akatundu, adzagawana cimodzimodzi.

25. Ndipo kuyambira tsiku lija kufikira lero lomwe anaika ici, cikhale lemba ndi ciweruzo pa Aisrayeli.

26. Ndipo pamene Davide anafika ku Zikilaga, anatumizako za zofunkhazo kwa akuru a Yuda, ndiwo abwenzi ace, nati, Siyi mphatso yanu ya zofunkha za adani a Yehova.

27. Anatumiza kwa iwo a ku Beteli, ndi kwa iwo a ku Ramoti wa kumwela, ndi kwa iwo a ku Yatiri;

28. ndi kwa iwo a ku Aroeri, ndi kwa iwo a ku Sifimoti, ndi kwa iwo a ku Estimoa;

29. ndi kwa iwo a ku Rakala, ndi kwa iwo a m'midzi ya Ayerameli, ndi kwa iwo a m'midzi ya Akeni;

30. ndi kwa iwo a ku Horima, ndi kwa iwo a ku Korasani, ndi kwa iwo a ku Ataki;

31. ndi kwa iwo a ku Hebroni, ndi kumalo konse kumene Davide ndi anthu ace adafoyendayenda.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 30