Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 3:17-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Ndipo anati, Anakuuza cinthu canji? Usandibisire ine. Mulungu akulangendi kuonjezapo, ngati undibisira cimodzi ca zonse zija adanena nawe.

18. Ndipo Samueli anamuuza zonse, sanambisira kanthu. Ndipo iye anati, Ndiye Yehova; acite comkomera pamaso pace.

19. Ndipo Samueli anakula, Yehova nakhala naye, osalola kuti mau ace amodzi apite pacabe.

20. Ndipo Aisrayeli onse, kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba anazindikira kuti Samueli anakhazikika akhale mneneri wa Yehova.

21. Ndipo Yehova anaonekanso m'Silo, pakuti Yehova anadziulula kwa Samueli ku Silo, mwa mau a Yehova.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 3