Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 3:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo mwanayo Samueli anatumikira Yehova pamaso pa Eli. Ndipo masiku aja mau a Yehova anamveka kamodzi kamodzi; masomphenya sanaoneka-oneka.

2. Ndipo kunali nthawi yomweyo Eli atagona m'malo mwace (maso ace anayamba cizirezire osatha kupenya bwino);

3. ndi nyali ya Mulungu isanazime, Samueli nagona m'Kacisi wa Yehova, m'mene munali likasa la Mulungu.

4. Pamenepo Yehova anaitana Samueli; ndipo iye anayankha kuti, Ndiri pano.

5. Ndipo anathamangira kwa Eli nati, Ndine, popeza mwandiitana ine. Ndipo iye anati, Sindinaitana, kagone. Napita iye, nagona,

6. Ndipo Yehova anabwereza kumuitana, ndi kuti, Samueli. Ndipo Samueli anauka, napita kwa Eli, nati, Ndine, pakuti mwandiitana ndithu. Koma iye anayankha, Sindinaitana, mwana wanga; kagone.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 3