Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 25:29-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

29. Ngakhale anauka anthu kukulondolani, ndi kufuna moyo wanu, koma moyo wa mbuye wanga udzamangika m'phukusi la amoyo lakukhala ndi Yehova Mulungu wanu; koma iye adzaponya miyoyo ya adani anu kuwataya monga coturuka m'coponyera mwala.

30. Ndipo kudzali, pamene Yehova anacitira mbuye wanga monga mwa zabwino zonse adalankhula za inu, ndipo adadzaika inu mukhale kalonga wa Israyeli;

31. mudzakhala opanda cakudodoma naco, kapena cakusauka naco mtima wa mbuye wanga, cakuti munakhetsa mwazi wopanda cifukwa, kapena kuti mbuye wanga anabwezera cilango; ndipo Yehova akadzacitira mbuye wanga zabwino, pamenepo mukumbukile mdzakazi wanu.

32. Ndipa Davide anati kwa Abigayeli, Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Israyeli, amene anakutumiza lero kudzandicingamira ine;

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 25