Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 23:25-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Ndipo Sauli ndi anthu ace anamuka kukamfuna. Koma wina anauza Davide; cifukwa cace anatsikira kuthanthweko, nakhala m'cipululu ca Maoni. Ndipo pamene Sauli anamva ici, iye anamlondola Davide m'cipululu ca Maoni.

26. Ndipo Sauli anamuka mbali yina ya phiri, Davide ndi anthu ace kutseri kwace; ndipo Davide anafulumira kuthawa, cifukwa ca kuopa Sauli; popeza Sauli ndi anthu ace anazinga Davide ndi anthu ace kwete kuti awagwire.

27. Koma mthenga unafika kwa Sauli ndi kuti, Mufulumire kubwerera; popeza nkhondo yobvumbulukira ya Afilisti yalowa m'dziko.

28. Comweco Sauli anabwerera polondola Davide, nakakomana ndi Afilisti; cifukwa cace anachula dzina lace la malo aja, Thanthwe lolekanitsa.

29. Ndipo Davide anakwera kucokera kumeneko, nakhalam'ngaka za Engedi.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 23